Kishore Kumar Hits

Billy Kaunda - Zachabechabe şarkı sözleri

Sanatçı: Billy Kaunda

albüm: Mwataya Chipangano (Agalatia)


Wandituma Chauta, wandituma
Kuti mkambe nanu anthu anga
Akuti za m'dziko nzachabe
Ati zonse tiziona leroli
Palibe chomwe ndi chachilendo
Zonsezi, zinalipo kalero
Kunali mafumu wolamulira
Akayankhula aliyese kumvetsa
Ali kuti lero? mudzifunse
Kunali asungwana wokongola
Kusekelera ngati asasiye
Ali kuti lero? mudzifunse
Kunali anyamata ovala bwino
Kuvala ngati asokera pompo
Ali kuti lero? mudzifunse

Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe
Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe
Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe
Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe

Ntchito za munthu zimasautsa
Kodi nanga apindula chani
Poti dzuwali, lingozungulirabe
Mitsinje ithira madzi m'nyanja
Nanga bwanji nyanja siyisefuka?
Kubwelera kwachokera mtsinjewo
Zinthu zonse zolemetsa mutu
Sangathe kufotokoza zonse
Maso sakhuta, satopa kuona
Makutu sakhuta nako kumva
Chomwe chinawoneka chidzawoneka
Chochitika, Chidzachitikanso
Za moyo uno nzachabechabe
Zimasintha kukondweletsa mtima
Atero mlaliki
Zili chabe

Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe
Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe
Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe
Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe

Chilichonse chili ndi nthawi yache
Nthawi yakubadwa ndi yakufa
Yodzala, ndi ya kudzula
Nthawi yakupha ndi yakuchiza
Yakupasula ndi yakumanga
Ya misozi ndi yakuseka
Pali nthawi ya munthu yolira
Ndipo pali ina yakuvina
Yomwaza, ndi yotolera
Msakondwe ndi nzeru ya padziko
Munzeru yambiri muli chisoni, chambiriso
Atero mlaliki
Mowonjezera nzeru awonjezera
Zowawa nzochuluka komanso
Kukhala chitsiru, sikwabwininso

Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe
Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe
Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe
Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe
Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe
Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe
Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe
Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe

Поcмотреть все песни артиста

Sanatçının diğer albümleri

Benzer Sanatçılar