Zikuwoneka ngati anthu oyipa
Achuluka kuposa abwino
Zikumawonekanso ngati
Anthu odziwa malemba
Achuluka kuposa owachita
Kuno zikumawonekanso ngati
Azitumiki anu ambiri
Nkhani ya chuma yawayanja
Zikumadza wonekanso ngati
Uthenga woti mudzabweranso
Padakali pano adawupumitsa
Ine nde ndimati mwina
Mtumeko angelo anu
Andipeze mu getsemani
Zikuwoneka ngati
Mwabwera malonda
Mnyumba mwanu
Zikuwoneka ngati
Pabisala achifwamba
Mnyumba mwanu
Nde tumani angelo anu
Angelo anu
Tumani angelo anu
Andipeze mugetsemani
Zikuwoneka ngati
Kwalowa akuba eh eh eh
Mnyumba mwanu
Zikuwoneka ngati
Pabisala achifwamba
Mnyumba mwanu
Koma zili mnyumba mwanu
Yehova mnyumba mwanu
Oh mnyumba mwanu
Alowetsamo kuba
Chigololo komanso malonda ah
Mnyumba mwanu
Kodi mmesa mumati simusintha
Dzulo dzana ndi mkuja
Inu muli yemwe uja
Mphamvu zanu zili pompaja
Mutha kukwapula anthu paja
Ngati munachitila kale lija
Mkachisi muja
Nanga lero bwanji
Mtumeko angelo anu
Adzawakwapule
Tati tumani angelo anu
Oh angelo anu
Zikuwoneka kuti
Anthu atopa ndi bodza
Lalowa mnyumba yanu
Zikuwonekanso kuti
Anthu akulizidwa koma
Mnyumba yanu
Ine nde ndimati mwina
Mtumeko angelo anu
Andillimbikitse
Tumani angelo anu
Andipeze mugetsemani
Zikuwoneka ngati
Mwabwera malonda
Mnyumba mwanu
Zikuwoneka kuti
Mwalowa chibwana
Mnyumba mwanu
Nde tumani angelo anu
Angelo anu
Tumani angelo anu
Angelo anu
Поcмотреть все песни артиста
Sanatçının diğer albümleri