Kishore Kumar Hits

Namadingo - Maury şarkı sözleri

Sanatçı: Namadingo

albüm: Maury


(Okay why?)
Namadingo
Kumvetsetsana
Inde tinkamvetsetsana
Ija inali true love
Tinkakondana ah ah ah
Zatsogolo lathu, zidali mmanja mwake
Mwa Mulungu
Koma yemwe adanena palibe chosatha
Sadanane zonse zimatha ah ah
Zimawawa palibe chamuyaya ah ah ah ah
Maury adandisiya
Maury adakwatiwa
Ine zidandiwawa koma
Ululu umatha ah ah ah
Pakapita nthawi ine
Mabala achila ah ah ah
Maury adandisiya komabe
Ululu umatha ah ah ah
Moyo goes on
Mabala achila ah ah ah
Palibe chamuyaya

Papita nthawi ine
Maury atandisiya
Maury adakwatiwa uh

Atapita Maury
Nalo dziko lidandikulira
Mtima kupweteka nkumangopirira, (kupirira)
Pagulu ukumwetulira
Kumbali ukusisima, ukulira
Maganizo kukumbukira momwe chikondi chinkakomera
Simomwe mtima wako nawonso umawawira
Kutopa ndi kulira maso kufila
Kufuna kudzimangirira ah ah ah
Koma ayi ayi uh huh
Zonse zimatha mchimwene wanga
Palibe chosatha mchemwali wanga
Zimawawa komabe
Ululu umatha ah ah ah
Papita nthawi komabe
Mabala achila ah ah ah
Ine Maury adandisiya
Komabe ululu umatha ah ah ah
Ndipo mabala achila ah ah ah
Maury adandisiya
Maury adakwatiwa
Palibe chosata ah ah ah
Ndipo palibe chamuya ah ah ah
Olo ndalama imatha
Iwe kukhala mmaludzi
Maudindo amatha
Iwe kukhala nobody
Olo maluzi amatha
Mutayipedza bandulo
Inu minyama imatha
Iwe kupedza mdalitso
Ungolimba mtima, (moyo ndi choncho moyo)
Tsiku lina udzachira, (moyo ndi choncho moyo)

Поcмотреть все песни артиста

Sanatçının diğer albümleri

Benzer Sanatçılar