Amangolira (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangorila (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ana anga inu
Ana anga inu
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ndikuvutika, ndikuzuzika inu mulipo
Taonani ndinakupatsani kamoyo kabwino, kokongola
Inu taonani ndinakupatsani tiana tabwino, tokongola
Koma nokha nokha mukumaphana
Mukumalimbana
Mukumatembelerana
Mukumaponderezana
Simukukondana
Mukumasalana
Mukumatamba
Chosecho manune kachitenje ndikamozi
Kamalaya ndikamozi
Ka bulangete ndikamozi (yah)
Amangolira (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangorila (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ana anga inu
Ana anga inu
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ndikuvutika, ndikuzuzika inu mulipo
Chumachi ndi changa
Magalimotowa ndianga
Mumapangira miyala yanga
Mafuta ndi anga
Ngakhare magetsi ndi anga
Zimapangidwa ndimadzi anga
Koma nokha nokha mukudzilengela matenda
Machilitso ndikumagulitsana
Ndinu akhwidzi
Muli ndizisisi, sisi, sisi, sisi, sisi, sisi, sih
Muli ndizisisi, sisi, sisi, sisi, sisi, sisi, sih
Amangolira
Amangolira (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangorila (mayi Malawi)
Walira (mayi Malawi)
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ana anga inu
Ana anga inu
Amangoti (ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Ndikuvutika, ndikuzuzika inu mulipo
Amandiseka azimayi azanga tikakumana kumagulu
Mai Malawi mumakhala ngati simunaberekepo inu
Amandidabwa azimai azanga tikakumana kumaguru
Mai Malawi mumakhala ngati simumamuopa mulungu
Komatu ife timakusilirani
Muli ndikanyanja kabwino
Muli ndimitsinje yabwino
Muli ndikanyengo kabwino
Muli ndika thaka kabwino
Muli ndizinyama zabwino
Muli ndimapiri abwino
Ana anu ndiopirila bwino
Nkona ndikakhala ndimagwada pansi
Kumpembedza Namalenga m'mwamba
Chonde mbuye dziko musalilange mulange ine monga kholo lawo
Oh, my God
Yah-yah, yah
(Mayi Malawi)
(Mayi Malawi)
Yaachina Seven adah
(Mayi Malawi)
(Mayi Malawi)
(Ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
(Ayi-ayi-ayi-ayi, ayi-ayi-ayi-ayi-ayi)
Поcмотреть все песни артиста
Sanatçının diğer albümleri