Kishore Kumar Hits

Phungu Joseph Nkasa - Mtima Mmalo şarkı sözleri

Sanatçı: Phungu Joseph Nkasa

albüm: Wayenda Wapenga


Msamatiponye inu eni ake achuma
Musamatiponye miyala
Nafenso ndi wanthu
Msamatitembelele m'malo motidalitsa
Joseph Mkasa akuti musamanyoze amphawi

Achuma nanu mudzilemekeza wosawuka
Tikamaswa nsabwe musamatiyese otembeleledwa
Tilibe zifukwa kapena mangawa ndi Mulungu
Mukamatiseka m'makhala ngati mukutidzudzula
Mabala a umphawi amene alibe ma dokotala
Sitimada nkhawa ife chachikulu nabola moyo
Chauta mwina ndiyemwe adziwa kusintha nyego
Ukasawuka usatenge chingwe kudzipha nacho
Ndikuwuzeni ngati munafika kwa Mayaka
Che Bauleni pa sitolo yawo analemba
Mukawelenga kuti zabwino zili mtsogolo
Mtima m'malo
Tafatsani
Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo
Usalire, nzanga osawuka
Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo
Tidzalemela ife
Tidzachita bwino
Tizangangalala, nthawi yathu izafika
Ndizolembalemba, nzolembalemba
Ndizosayinasayina
Zonse zidikira nyengo

Anzanu ena anachita mwano posamuka
Anamenya anthu, kutukwana mfumu m'mudzi muno
Mbewu ku dimba adakapopela poison
Kutsilika minda kuti atalime awone mbwadza
Anakumba munsewu ndi mulata adawuthyola
Kunali chi ngongole ku kalabu anathawitsa
Anadula minga kukayiwunjika pa m'jigo
Anasiya anthu atawawombanitsa mitu
Anayiwala kuti chawuluka chizatela
Ntchetche inati mtsogolo moyo m'mbuyo moyo
Mtima m'malo
Tafatsani
Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo
Usalire, nzanga osawuka
Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo
Tidzalemela ife
Tidzachita bwino
Tizangangalala, nthawi yathu izafika
Ndizolembalemba, nzolembalemba
Ndizosayinasayina
Zonse zidikira nyengo

Mtima m'malo
Tafatsani
Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo
Usalire, nzanga wosawuka
Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo
Tidzalemela ife
Tidzachita bwino
Tizangangalala, nthawi yathu izafika
Ndizolembalemba, nzolembalemba
Ndizosayinasayina
Zonse zidikira nyengo

Mtima m'malo
Tafatsani
Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo
Usalire, nzanga wosawuka
Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo
Tidzalemela ife
Tidzachita bwino
Tizangangalala, nthawi yathu izafika
Ndizolembalemba, nzolembalemba
Ndizosayinasayina
Zonse zidikira nyengo

Mtima m'malo
Tafatsani
Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo
Usalire, nzanga wosawuka
Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo
Tidzalemela ife
Tidzachita bwino
(Tizangangalala, nthawi yathu izafika)

Поcмотреть все песни артиста

Sanatçının diğer albümleri

Benzer Sanatçılar